![Siyabonga iNkosi Ganya Hlabathi 🙏](https://img3.evepla.com/471/780/514369924717802.jpg)
11/10/2024
Siyabonga iNkosi Ganya Hlabathi 🙏
iNkosi Ganya ya m’boma la Ntcheu yati nkhani zokwatitsa ana ndi mbiri yakale mdera lake kaamba ka malamulo ang’onoang’ono okhwima omwe anawakhazikitsa polanga onse okolezera ma ukwati a ana.
A Ganya ati mwa chitsanzo , chaka chino ma ukwati a ana awiri okha ndi omwe awathetsa kuyerekeza ndi maukwati oposa 70 omwe iwo pamodzi ndimafumu awo anathetsa mchaka cha 2021.
Mfumuyi yalankhula izi lero ku likulu lake la Mtudza lomwe liri ku dera la Kandeu pa mwambo wa umhlangano wa Angoni omwe ali pansi pake komwe yati ntchito yobwezeretsa chiyankhulo cha ISiNgoni iyambiranso mderalo.
Pakadali pano, wapa mpando wa khonsolo ya boma la Ntcheu, Flaness Kampeni wati zomwe ikuchita mfumuyi zifalikiranso madera a mafumu onse akuluakulu khumi ndi cholinga choteteza ana ku nkhaza zowakwatiwitsa.
Mwambo wa umhlangano wa Angoni a Maseko omwe ali pansi pa iNkosi Ganya unayamba mchaka cha 2012 ndicholinga chosunga mbiri komanso kulimbikitsa chikhalidwe cha angoni a mtunduwu mderalo.
(by Blessings Kang’ombe-Ntcheu:10/11/24)