03/10/2023
A utumiki wa Salvation For All Ministries Motsogozedwa ndi Apostle Clifford Kawinga akukudziwitsani zakusintha kwa Masamba awo apa internet kutsatila kubedwa kwa page lawo la Facebook, lomwe anthu ena awupandu akuligwilitsa ntchito mosayenera.
Choncho Utumikiwu ukukudziwitsa nonse omwe mumatsatira zochitika za utumikiwu kudzera patsamba lakale lotchedwa "Apostle Clifford Kawinga Ministries" kuti kuyambira pa 15 June 2023, tsambali linabedwa ndipo sililinso mbali imodzi ya utumikiwu. Kotero mukupemphedwa kuyamba kutsatila page latsopano lomwe ndi "Apostle Clifford Kawinga Ministries Official'
Mukafuna kudziwa zambiri yankhulani ndi Mr Chipeni, Mkulu wazofalitsa nkhani Ku utumikiwu 0997923754/ 0882489294 of [email protected]